Potsatira maphunziro, omwe anali nawo mwezi wa May okhudza kapangidwe kamakala ochokera kuzinyalala, achinyamata a gulu la Kafoteka mu boma la Mzimba ayamba kupanga paokha makalawa.
Guliri, lomwe limachokera m’mudzi mwa Inkosi Mmbelwa, lati atachita maphunziro wa kwatsiku limodzi anaona kuti ndiokwanira ndipo sanafune kuchedwa kuyamba kupanga makalawa.
Mwayi Makhala ndi wapampando guluri iye wati upangiri omwe Anthony Botha ndi anawapatsa okwanira kupanga zinthu zambiri, mwazina iwo ati makalawa akauma akuyembekezera kuzapeza ndalama zochuluka komanso adziphikira okha.
“Tikagulitsa makalawa athandiza kuti ntchito za gulu yathu zipite pa tsogolo komanso miyoyo yathu isintha ndithu, till ndi amzathu omwe akuphunzirabe sukulu ndipo azitha kupeza zosowa pa moyo wa sukulu kudzera mu ichi” anafotokoza Makhala.
Iwo ati kupita chitsogolo akufuna aziphunzitsa achinyamata komanso azimayi kapangidwe kamakalawa kuti naoso akhale ozidalira paokha pachuma mbali inayi akuteteza chilengedwe.
“Koditu ngati sitipanga izi nkumadalira Makala kwinako mitengo izatithera tizasowa kolowera ndi bwino anthu tiphunziretu kugwiritsa ntchito ma briqquetes poteteza chilengedwe”Makhala anatero.
Mau ake Anthony Botha yemwe akuphunzitsa achinyamata wati ndiokondwa poona kuti ntchito yake zayamba kubala zipatso ndipo wati achilimika kufikira aliyese mu boma la Mzimba.






