NAMONDWE BHEKI WABADWA M’NYANJA YA MCHERE YA INDIA

Namondwe Bheki wabuka m’nyanja ya mchere ya India masiku atatu apitawo.

Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo m’dziko muno yati pakadali pano Namondweyu ali kutali ndi chilumba cha Madagascar ndi mtunda wa makilomita opitilira zikwi ziwiri (2,000) cha kumvuma kwa chilumbachi.

Malingana ndi Chikalata cha nthambiyi, namondweyu akuyenda pa liwiro la 12 makilomita pa ora limodzi kulunjika gombe ya chilumbachi.

Apa, nthambiyi ikumemeza anthu m’dziko muno kuti adzitsatira maulosi otsimikizika omwe nthambiyi imapereka pofuna kupewa chisokonezo.

Polankhula ndi anthu m’boma la Nsanje, Grace Dzowa ayamikira Nthambi Yoona za Nyengo ndi Kusintha kwa Nyengo podziwitsa a Malawi za Namondwe.

“Ndidzikhala tcheru kumvera malipoti omwe Nthambiyi idzitulutsa pofuna kukhala okonzeka,” atero Dzowa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *