TIMU YA MPIRA WA MANJA YA SENA MODELS YA KU NSANJE AYIYAMIKIRA

Timu ya mpira wa manja ya Sena Models ndi yokhayo yomwe idayamba kusewera kalekale m’boma la Nsanje.

Peter Mizedya yemwe ndi m’phunzitsi wa timuyi wati, timuyi idayambitsidwa kaamba ka kolowerera kwa atsikanawa.

Iwo ati mudali mu chaka cha 2012 pomwe atsikana analowera kwambiri mpakana osamafuna kuphunzira.

Mizedya wauza ProjectM kuti yemwe adali Mkulu wa Polisi m’bomali, Assistant Commissioner of Police (ACP) Sekani Tembo, anatenga gawo lalikulu polimbikitsa atsikana kuti akhale ndi khalidwe labwino.

“Njira yomwe tidatsata linali loyambitsa timu ya mpira wa manja yomwe ACP Tembo amayithandiza kwa zaka zitatu,” adatero Mizedya.

Iwo ati mayi Tembo atachoka ku Nsanje timuyi idasowa oyithandiza ndiponso dzina la Police lidathera pomwepo.

Pa za dzina la Sena Models, mphunzitsiyu wati kwenikweni dzinali lidadza potsatira kusintha kwa makhalidwe atsikanawa ndipo ichi chinali chitsanzo chabwino kwa ena.

Iye wati atsikanawa akumachita nawo zachikhalidwe cha makolo potengapo gawo pa magule monga: utse, chikuzile, maseseto mwa ena chabe.

Pamenepa, a Mizedya ati chaka ndi chaka timu ya Sena Models imatenga nawo pazochitika za Khulubvi Arts and Cultural Festival.

Mfumu yaikulu Chimombo m’bomali yati timu ya Sena Models ndi yachitsanzo mu Nsanje.

Iyo yatinso yakhala ikuona asungwanawa akutenga mbali pa mwambo otukula chikhalidwe wa Khulubvi Arts and Cultural Festival.

“Sibwino kusochera mwa dala pomwe otiphunzitsa za makolo athu alipo,” idatero mfumu yaikuluyo.

Mfumu yaikulu Chimombo yapempha asungwana ena ku Nsanje kuti atengere khalidwe la timu ya Sena Models yomwe ndiyosangalatsa kwambiri.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *