Bungwe la Shire Valley Transformation Programme (SVTP) yati ndiyochilimika potenga mbali yayikulu posamalira za chilengedwe m’malo onse m’mene mudutse ngalande za madzi maboma a Nsanje ndi Chikwawa.
Mkulu wa SVTP a Stanley Chakhumbira Khaila wanena izi Lachitatu ku Nsanje pomwe amakumana ndi mamembala a khonsolo m’bomali.
Iye wati SVTP idayamba kusamalira za chilengedwe m’malo momwe mudutse ngalande zodzapereka madzi ku minda ya alimi.
A Khaila auza ProjectM kuti pakadali pano ntchito za SVTP zomanga ngalande sizidafike m’boma la Nsanje.
Mkulu wa SVTP adatinso anthu a maboma awiriwa aphunzitsidwa za m’mene angatetezere za chilengedwe m’malo momwe mudutse ngalandezi.
“Anthuwa adapatsidwa mbuzi zomwe n’zopatsirana ngati njira imodzi yowalimbikitsa kuti asaononge malo otetezedwa a Lengwe, Majete ndi Mwabvi,” adatero a Khaila.
Iwo adaonjezera kuti kupatula kupereka ziweto anthu aphunzitsidwanso ulimi wa njuchi pofunitsitsa kuti asamadule mitengo chisawawa.
Pamenepa mkuluyu adanenanso kuti Gawo limodzi la SVTP la Global Environmental Facility (GEF) njomwe ikuonetsetsa kuti zachilengedwe zitetezedwe.
“Dambo la Elephant mu Nsanje muno lili ndi zambiri zokopa alendo monga: mbalame ndi mvuwu moti GEF ikugwira ntchito yotamandika poteteza zachilengedwe,” adatero a Khaila.
Mfumu Yayikulu Chimombo yapempha a SVTP kuti adzatenge mamembalawa kuti akadzionere okha pa ntchito yomwe ikugwiridwa.
“Ndi pempho lathu kuti mudzatitengere ku Chikwawa komwe tikaone ngalande zodzapereka madzi ku minda ya alimi,” idatero mfumuyi.
Ntchito ya Shire Valley Transformation Programme ikadzatha idzasintha miyoyo ya anthu maboma a Nsanje ndi Chikwawa pa chakudya ndinso pa chuma.