RODWELL LUMBE APITILIZA KUFIKIRA ANTHU A ULUMALI

Wachinyamata yemwe amadziwika ndi ntchito zachifundo mdziko muno Rodwell Lumbe wati mwambo wa Christmas luncheon uliko chaka chino.

Uwu ndi mwambo omwe umachitika chaka ndi chaka omwe ati cholinga chake ndikufuna kufikira anthu amaulumali osiyanasiyana pokwendwelera chikondwelero cha Christmas.

Polemba patsamba lake la mchezo Rodwell wati mu zaka ziwiri zomwe wakhala akugwira ntchitoyi wakwanitsa kufikira anthu amaulumali Okwana 3000.

“Timakonza mwambowu ndicholinga chokhala nawo limodzi azathu a ulumali potengera kuti ndi anthu amene amazimva kusalidwa komaso kusawerengedwa kwambiri mu zinthu zochitika zosiyanasiyana mdziko muno” anafotokoza motero Rodwell.

Ku mwambowu kumakhala madyelero, kulimbikitsana moyo wathanzi komaso kutukula ma bizinesi ndima luso komaso maupangiri osiyasiyana.

“Chaka Chino mwambowu uchitikira Ku Lilongwe mu mwezi wa disembala koma tsiku ndi Malo tizilengezabe mtsogolomu’ anatero a Lumbe

Iye wapitiliza kupempha anthu akufuna kwabwino kuti athandizepo ndi chakudya, ndalama komaso kusankhapo munthu mmodzi yemwe angamutukule bizinesi yake.

Mau Ake Saube Kandeu yemwe ndioimba waulumali ndipo pamwambo wachaka Chatha anasangaltsa anthu ndi nyimbo zake wati ndiokonzeka kusangalatsa anthu mmaimbidwe ake Ku mwambo wachaka Chino ngati ataitanidwe.

Chaka Chatha mwambo ngati omweu unachitikira mu mzinda wa Blantyre.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *