NTCHITO YOMANGA SUKULU YA MPATSA PULAYIMALE IYAMBA POSACHEDWA

Mkulu wa bungwe loona za mavuto odza mwadzidzi m’dziko muno la Department of Disaster and Management Affairs (DoDMA), Commissioner Charles Kalemba atsimikizira anthu a m’dera la Mfumu Yayikulu Tengani m’boma la Nsanje kuti ntchito yomanga sukulu ya pulayimale ya Mpatsa iyamba posachedwa m’derali.

Iwo anena izi Lachisanu atayendera malo a tsopano pomwe pamangidwe sukulu ya tsopano.

A Kalemba auza ProjectM kuti ndalama zokwana K225 million za ntchito zilipo nzochokera mu thumba lapadera la mtsogoleri wa dziko lino (Presidentary Charitable Initiative).

“Tiyamba kumanga midadada iwiri, ofesi ndinso zimbudzi ziwiri,” atero a Kalemba.

Mkuluyu atinso Nthambi yake ikumba mjigo pofuna kuonetsetsa kuti madzi asakhale vuto pogwira ntchito yomanga sukulu.

Phungu wa m’dera la Pakati m’boma la Nsanje, Kafandikhale Mandevana athokoza boma pobweretsa chitukukochi munthawi yake pomwe ophunzira akusowa malo abwino ophunziramo.

Iwo alonjeza kuti aonetsetsa kuti ntchitoyi iyende mwamsanga ndipo ngati pangakhale vuto lililonse ndilowerapo.

“Ndiyetsetsa kuti mthumba la ndalama zachitukuko cha ku mdera la Constituency Development Fund (CDF) angakhale mthumba la Chitukuko la Boma la District Development Fund (DDF) zithandizire pomanga sukulu ya tsopanoyi,” adatero phunguyu.

Nyakwawa yayikulu Chisi yati ngosangalala kuti tsopano malo omangapo sukulu atsimikizika.

.”Ana athu akhala alikuvutika kwambiri palo awo ongogwilizira pomwe akuphunzilirapo,” adatero Nyakwawa yayikulu Chisi.

Mphunzitsi wamkulu wa Mpatsa Pulayimale, a Jussab Mintrozo ati kwake mkunyadira kuti sukulu ya tsopanoyi ichepetsa mavuto omwe akumana nawo pa malo ogwirizirawa.

Pa sukulu ya pulayimale ya Mpatsa pali ophunzira 2,871 ndi aphunzitsi 27.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *