MKULU WA APOLISI KU CHIKWAWA AMEMA AMAYI KULEWA NKHANZA

Mkulu wa a polisi m’boma la Chikwawa Assistant Commissioner of Police (ACP) Carolyn Jere amema amayi kuti akhale a chikondi poonetsa mtima wa chikondi waunakubala popewa nkhanza za mtundu uliwonse.

A Jere ati apolisi a akazi kwa masiku atatu akhala ali kupereka chitetezo chomwe chimatchedwa “Basadi.’

Iye auza ProjectM kuti ngati njira imodzi yothokoza ntchito yayikulu yomwe amayi amagwira anaganiza zopereka mphatso zosiyanasiyana kwa amayi pa chipatala chachikulu cha Chikwawa.

“Tinalunjika kwa amayi amene angobereka kumene kuti athandizire kusamalira miyoyo ya ana ongobadwa kumenewa,” adatero mkuluyu.

M’modzi mwa amayi omwe alandira thandizoli Doreen Haji athokoza a Polisiwa powapatsa mphatso zomwe iwo samayembekezera.

“Si chapafupi kuti anthu ena aganizire enanso malingana ndi nyengo zino,” adatero mayiyu.

A Maxwell Yambeni, m’modzi mwa ogwira ntchito pa chipatala cha chachikulu cha Chikwawa ayamikira a Polisiwa ponena kuti mphatso zabwera nthawi yake pomwe amayi akusowa pogwira.

“Mphatso zithandiza kutukula ukhondo ndi thanzi kwa odwala,” adatero a Yambeni.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *