KUSAMALA IPHUNZITSA ATOLANKHANI ULIMI WA MAKOLO

Bungwe la Kusamala Institute of Agriculture and Ecology lalimbikitsa atolankhani m’dziko kugawa uthenga olimbikitsa ulimi ogwiritsa ntchito mbeu komaso njira zamakolo uja pa chingerezi amati organic.

Iwo anena izi pa mkumano omwe anakonza ku Lilongwe ndipo mkumanowu unabweretsa pamodzi atolankhani ochokera m’zigawo zonse m’dziko muno.

Dorothy Limbanga, yemwe ndi mkulu oyang’anira ntchito ku bungweli wati ulimi ogwiritsa ntchito njira zamakolo uli ndikuthekera kothetsa njala komanso umphawi m’dziko muno.

“Ulimiwu ndi opindulitsa komanso sufuna zambiri. Masiku ano feteleza anakwera mtengo ndiye yafika nthawi tsopano kuti alimi ayambe kugwiritsa ntchito njira zopezekeratu monga manyowa a mitundu yosiyanasiyana kuphatikizapo mkodzo wa munthu, tikatero ndekuti tidzapulumutsa ndalama ya feteleza,” anatero Limbanga.

Iwo atinso pambali pogwiritsa ntchito manyowa, alimi atha kumadzipangira okha mankhwala othana ndi tizilombo tilitonse tomwe tingakhudze mbewu zawo posagwiritsa ntchito  mankhwala ogula m’sitolo.

Bungweli linaonjezeraso kunena kuti mbeu zambiri zamakolo zimapilira kunyengo zosiyanasiyana ndipo mlimi atha kupanga phindu pamene kungakhale kuti kwagwa milili yosiyana siyana.

“Ndikusintha kwa nyengo ndibwino kudalira mbeu zimene tikudziwa kuti zitha kuchita bwino zitakumana ndinyengo zosiyanasiyana, tikatero mbiri ya njala izakhala nkhambakamwa chabe,” anaonjezera Limbanga.

Iwo apemphanso adindo osiyanasiyana kutengapo gawo polimbikitsa ulimi wa njira za makolo.

Khumbo Chiudzu m’modzi mwa atolankhani yemwe anali nawo pa maphunzirowa, wati maphunzirowa abwera mu nthawi yake pomwenso tikuyandikira nyengo ya mvula ndipo ayesetsa kukonza ma pulogalamu komanso kulemba nkhani zokhudza ulimiwu.

“Ubwino waulimiwu taona kuti alipo ambiri potengera kuti si ulimi oti umalira mvula yokhayokha, monga ife aulutsi tili ndikuthekera kopitsa patsogolo ulimi wamakolowu” Chiudzu anatero.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *