Gulu la Malawi National Dance Troupe likuyembekezeka kukayimba m’dziko la Japan pa mwambo wa Japan World Expo 2025 mwezi uno wa June.
Gululi lati ndilokondwa ndi losangalala chifukwa chopeza mwayi ngati umenewu okayimba m’dziko la Japan.
M’modzi wa gululi, James Thole wawuza ProjectM kuti gululi linanyamuka m’dziko muno Loweruka pa 14 June.
Malingana ndi Thole, gulu la Malawi National Dance Troupe likuyembekezera kukaonetsa magule akuno monga Chisamba, Manganje ndi Vimbuza.
“Magulewa ndi njira imodzi yoonetsera chikhalidwe chathu chachiMalawi,” atero mkuluyu.
Thole aonjezera kunena kuti magulewa akawaonetsedwa pa 18 June.
