Gulu la amai la Sara mu mpingo wa Living Waters International, nthambi ya pa Bangula adachezera wodwala pa chipatala cha Kalemba mu nyengo ya chikondwerero cha Khisimisi.
Mai Mbusa Priscilla M’bwana ati adachiwona choyenera kukachereza odwala omwe sakadatha kukhala ndi achibale awo.
Mai m’busa M’bwana wawuza ProjectM kuti amai a Sarah anafikira odwala pa chipatala cha Kalemba ndipo ngokondwa kuti khumbo lawo lakwanilitsidwa kufikira odwala.
“Thandizo la ndalama tinalipeza kudzera mu ‘Paper Sunday’ yomwe tinapangitsa ndipo akhrisitu amipingo ina anabwera.
Mwapadera tikuthokoza Phungu wa dera la Nsanje Lalanje a Gladys Ganda ndi a Lawrence Sitolo potithandizanso,” atero Mai Mbusawa.
Wachiwiri kwa mkulu wa chipatala cha Kalemba Sr. Maureen Chalamanda athokoza amai a Sarah chifukwa cha chikonzero chawo chodzachezera odwala pano pa nyengo ino.
Iye wati samayembekezera kuti gulu la amai a mpingo wa Bangula Living Waters International angadzaone odwala.
“Mphatso apereka kwa odwala ziwathandiza mu njira zosiyanasiyana zomwe ayembekezera kulandira lero,” atero wachiwiri kwa mkuluyu.
M’modzi mwa opindula Alinafe Zuze wa zaka makumi awiri (20) ati ngonyadira ndi mphatso yomwe apatsidwa.
“sopoyi indithandiza kwambiri kuchapira matewera akhanda langa,” adanenetsa Zuze.


