ALIMI ADZAPEZA PHINDU NDI ULIMI WAM’THILIRA WA SVTP

Alimi a m’dera la mfumu yayikulu Kasisi m’boma la Chikwawa akuyembekezera kudzapeza phindu lochuluka pa ulimi wam’thilira kuyambira mwezi wa June chaka cha m’mawa kudzera pansi pa Shire Valley Transformation Programme (SVTP).

Mlembi Wamkulu wa Mwanaalirenji Koparetive a Tereza Mwalija ati alimi ayembekezere kudzapeza phindu kuchokera pa ulimi wa mbewu zomwe adasankha kulima.

A Mwalija auza ProjectM kuti alimiwa adzalima mbewu za soya, nyemba, tsabola ndi thonje zomwe adati misika yake ilipo kale.

Iye ati malo a Mwanaalirenji Koparetive ngokula mahekitala 774 ndipo alimi ali okonzeka kuyamba ulimi wam’thilira.

Mlembi Wamkulu adaulura kuti Boma lidathandiza ndi ndalama zokwana K10 biliyoni ngati yoyambira pa Koparetive pomwe pali alimi 791.

“Mwa chiwerengerochi (791) muli alimi 30 omwe ngaulumali ndipo akuyembekezera kudzapeza nawo phindu,” adatero mlembi wamkulu.

Wachiwiri kwa Mkulu wa SVTP, a Limbani Gomani adati gawo loyamba la ntchito yatha tsopano.

Iye ati chatsalira ndi madzi kuti afikire minda ya alimiwa kuti ayambepo ulimi wam’thilira.

Wachiwiri kwa Mkuluyu atsimikira alimiwa kuti pomadzafika mwezi wa June,2025 adzakhala tayamba ulimi wam’thilira.

Shire Valley Transformation Programme lakhazikitsa makoparetive khumi ndi atatu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *