M’modzi mwa achinyamata omwe akugwira ntchito yofuna kuteteza chilengedwe m’boma la Mzimba Anthony Botha wayamba ntchito yophunzitsa achinyamata kapangidwe kamakala otchedwa ‘briquettes’ m’chingereezi.
Botha yemwe akugwira ntchitoyi mongodzipereka wati anachiona chanzeru kuphunzitsa achinyamatawa potengera kuti achinyamata ali ndi udindo waukulu oteteza chilengedwe komanso kuti akhale odzidalira paokha akamagulitsa Malawi.
“Achinyamata ambiri amaganiza kuti kusamala chilengedwe ndi ntchito ya akuluakulu, ndiye ndibwino kuwazindikiritsa kutero. Ineyo ndidzipereka kuyendera ma dera onse kuno Ku Mzimba” watero Botha.
Botha wati kusowa kwa chithandizo cha ndalama ndi vuto lalikulu lomwe akukumana nalo ndipo akupempha akufuna kwabwino kuti amuthandize ntchitoyi.
Pakadali pano iyeyu wafikira achinyamata a club ya Kafoteka mubomali ndipo wati ndikhumbo lake kuti pomatha miyezi ikubwerayi akhale atamaliza ntchitoyi ndikuyambaso ntchito zina.
M’modzi mwa yemwe wapindulapo Amos Mwenda wayamikira maphunzirowa ponena kuti amutsegula m’maso ndipo panopa azipanga yekha makalawa omwe akupangidwa kuchokera Ku zinthu zosiyanasiyana.




