MAYI WAMALONDA AKWANITSA KUTUKUKA KUDZELA MU MALONDA OGULITSA TIYI

Mayi Elifa Letiya aku Mitundu m’boma la Lilongwe ndi chitsanzo chabwino pakati pa amayi anzawo atakwanitsa kusintha moyo wawo pankhani za chuma kudzera mu malonda ogulitsa tiyi.

Kwa nthawi yaitali, Mayi Letiya akhala akuchita malonda ogulitsa tiyi komanso ma sikono pa nsika wa Mitundu m’bomali.

Mayiwa awuza ProjectM kuti kumathero a chaka chatha, iwo adaganiza zoyamba kusungira gawo la phindu lomwe amapeza kudzera ku malonda ogulitsa tiyi ndi cholinga chofuna kupangira ulimi.

“Ngakhale ndakhala ndikugulitsa tiyi kwa nthawi yaitali, phindu lenileni silimaoneka kaamba koti ndalama yochuluka imathera kudyetsa banja langa ndiye izi zinanditopetsa,” mayi Letiya anatero.

Atakwanitsa kusunga ndalama zokwanira, mayiwa adayamba ulimi wa m’thilira miyezi yapitayo pomwe adalima mbewu zosiyanasiyana.

“Ndidakwanitsa kulima dimba lalikulu lomwe ndidalimamo mbeu monga Chimanga, Tomato komanso Mbatatesi,” anatero Mayi Letiya.

Kudzera mu zokolora zawo, Mayi Letiya adakwanitsa kupeza phindu lochuluka lomwe lina mwa phinduli adakwanitsa kuligwiritsa ntchito pokulitsa malonda awo ogulitsa tiyi.

Iwo anawonjezeranso ponena kuti pofika mwezi wa December chaka chino, pali chiyembekezo kuti akhoza kukololanso matumba pafupifupi makumi asanu a Chimanga chaku dimba chomwe analimanso miyezi itatu yapitayo.

Ndipo chidwi cha Mayi Letiya pankhani za malonda chinapangitsanso kuti bungwe la boma lobwereketsa ndalama la National Economic Empowerment Fund (NEEF) liwabwereke mpamba wa malonda okwana k1.5 million.

Malingana ndi mkulu wa bungwe la NEEF, Humphrey Mdyetseni, izi zidachitika pofuna kuti mayiwa apitirize kukhala chitsanzo chabwino pakati pa amayi anzawo.

“Mdziko muno n’zosowa kupeza amayi a masomphenya ngati momwe alili mayi Letiya ndiye ife ngati NEEF zidatipatsa chidwi,” anatero a Mdyetseni.

Pakadali pano, Mayi Elifa Letiya ati masomphenya awo ndiwofuna kukhala ndi Munda waukulu omwenso ungapangitse kuti azikolora mbeu zochuluka.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *