Bungwe la Churches Action in Relief and Development (CARD) alipempha kuti lifikire madera ena omwe ngovuta kufikilika ndi uthenga wuchimbere wabwino.
Izi zithandiza kupewa kutenga mimba pakati pa atsikana achichepere.
Nyakwawa Yayikulu Kanyimbi ya m’dera la Mfumu Yayikulu Tengani m’boma la Nsanje yanena izi pa sukulu ya pulayimale ya Chilunda pomwe bungweli limadziwitsa anthu za uchembere wabwino.
Nyakwawa yayikulu Kanyimbi yauza ProjectM kuti madera ambiri ku derali ngotalikirana potero uthenga wauchimbere wabwino sakuwafikira mokwanira.
“Madera anyakwawa Alindiamao, Kawa,Phaso mwa ena chabe ngotalikirana ndipo anthu aku maderawa sadakhale nafe pano paichi mauthengawa sadawapeze konse,” idatero nyakwawayi.
Mkulu wa bungwe la CARD Jemimah Phiri adati bungwe lake linapeza lipoti lakafufuku la ofesi yachisamaliro cha anthu ku Nsanje lomwe likuwonetsa kuti atsikana akutenga mimba komanso kulowa m’banja ali achichepere.
Iye ati kutenga mimba kwa atsikana achichepere kumapereka chiopsezo pa miyoyo yawo mwina atha kudwala matenda a kadza mkodzo pachingerezi fistula.
Pamenepa, a Phiri alonjeza kuti aonetsetsa kuti uthenga wauchembere wabwino ufikire madera onse momwe bungwe la CARD likugwiramo ntchito zake.
CARD likugwira ntchito zake madera amafumu akulu a Ndamera ndi Tengani m’boma la Nsanje.
Bungwe la Royal Norwegian Embassy likupereka thandizo la ndalama zokwana K1.4 billion zogwilira ntchito kwa zaka zitatu ma boma a Nsanje, Chikwawa ndi Machinga kudzera mabungwe a NorwegianChurch Aid ( NCA)/DanChurch Aid (DCA).