Akuluakulu omwe akuyendetsa zokonzekera zokhudza mwambo wa chikhalidwe cha a Tonga omwe umadziwika kuti Mdauku wa Tonga ati zokonzekera zili m’chimake kuti mwambowu uchitike m’mwezi wa August.
M’modzi mwa akuluakulu omwe akuyendetsa zokonzekera za mwambowu Goodwin Njikho wauza ProjectM kuti mwambowu udzachitika kuyambira pa 17 mpaka pa 18 August chaka chino.
Iwo ati padakali pano akambirana ndi magulu onse okhudzidwa kuti ayambe kukonza bwalo lomwe kukachitikire mwambowu.
“Tili okondwa kuti zokonzekera zonse zikuyenda bwino komanso anthu ochita malonda osiyansiyana kuphatikizapo ma bungwe atigwira manja ndipo tili ndi chikhulupiliro kuti mwambowu chaka chino uyenda bwino kwambiri,” anatero a Njikho.
Iwo apempha anthu okhala m’bomali kuti abwere mwaunyinji ponena kuti chaka chino ayembekezere kukhala ndi mwambo wopambana.
“Nthawi yakwana yoti anthu aphunzire zambiri za mtundu wa a Tonga, ku mwambowu takonza zinthu monga magule a makolo athu monga chilimika komanso malipenga, kungotchulapo ochepa komaso anthu adzakhala ndi mwayi odya zakudya zomwe makolo athu ankadya monga Nsima ya kondoole ndi ndiwo zake nkhungu,” A Njikho anaonjezera.
A Njikho apempha akufuna kwabwino kuti apitirize kuwathandizabe kuti mwambowu udzakhale opambana kwambiri.
Mwambowu umachitika chaka ndi chaka ndipo chaka chino mwambowu wakonzedwa pa mutu oti “Umodzi”.